Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

MUST ichititsa chionetsero cha chikhalidwe

Sukulu ya ukachenjede ya MUST m’boma la Thyolo yakonzeka kuchititsa chionetsero cha chikhalidwe, kafukufuku ndi luso cha chaka chino, kuchokera pa 4 mpaka pa 5 October. 

Ichi chikhala chionetsero chachiwiri kuchoka pomwe anakhazikitsa zochitikazi chaka chatha.

Malinga ndi mkulu wa zamaphunziro a chikhalidwe ku MUST, Atikonda Mtenje-Mkochi, chiyembekezo chawo ndi chakuti chionetserocho chithandiza kuti luso lomwe likugwirizana ndi chikhalidwe likhale laphindu pa chitukuko cha dziko lino.

Mwazina, pa chionetserocho padzakhala zoimbaimba za akatswiri monga Jetu.

Mutu wa chionetserocho chaka chino ndi Chikhalidwe: Nsanamira ya Chitukuko.

Related posts

Trust fund unveils K43BN Hotel project in Blantyre

MBC Online

Lumbadzi Police arrest woman of suspected infanticide

Romeo Umali

Centenary Bank partners with Tourism Ministry

Yamikani Simtowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.