Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Ubale wa dziko la China ulimbikitse Malawi pa ntchito zamalonda’

Sipikala wanyumba yamalamulo a Catherine Gotani Hara ati dziko lino litengerepo mwayi paubale omwe ulinawo ndi dziko la China popititsa patsogolo ntchito zamalonda.

A Hara anena izi ku Lilongwe kutsatira kubwera kwa wachiwiri wa sipikala wa nyumba ya malamulo yadziko la China, a Cai Dafeng.

Malinga ndi a Hara, nyumba yamalamulo ndiyodzipereka kukonza malamulo komanso kupanga ena amene angathandizire nkhani zamalonda m’dziko muno.

Pakali pano dziko la China, mwazina, likugula fodya komanso soya m’dziko muno, zomwe a Hara ati ndizothandiza kupititsa patsogolo chuma chadziko lino.

Mwazina, a Dafeng anayendera nyumba yamalamulo yadziko lino,imene inamangidwa ndithandizo lochoka kudziko la China.

 

Related posts

Mbava ipempha chilango chofewa chifukwa anayigulula mano

Rabson Kondowe

DPP impressed with by-elections performance

Chisomo Break

Puma partners Blue Elephants in symbiotic deal

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.