Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Amuna ambiri kumpoto akudwala khansa ya chida cha abambo

Akuluakulu apa chipatala chachikulu cha Mzuzu ati chipatalachi chikulandira abambo pafupifupi 60 mwezi uli ofuna chithandizo cha nthenda ya khansa ya chida cha abambo, penile cancer mchingerezi.

Malinga ndi Dr Alex Khombedza yemwe amayang’anira ntchito zamdulidwe pa chipatalachi, ambiri mwa abambowa ndi ochokera mzipatala zosiyanasiyana m’chigawo chakumpoto ndipo amafika zinthu zitaonongeka kale kaamba koti nthendayi imayamba ndi timatuza tomwe timanka tikula kutsogolo kwa chida cha abambo.

Dr Alex Khombedza, Mzuzu Central Hospital

Pa tsiku, chipatalachi chimalandira odwala matendawa awiri kapena atatu ndipo Dr Khombedza ati mdulidwe ndi njira yomwe ingathandize polimbana ndi vutoli.

Iwo amalankhula pamaphunziro a olembankhani m’chigawo chakumpoto amene anakonza ndi bungwe la JournAids linakonza ku Mzuzu.

Olembankhani omwe anatenga nao gawo pa maphunzirowa

Pakanali pano katswiri pa nkhani za umoyo George Jobe wati mpofunika kuti ma uthenga okhudza nthendayi afikile pali ponse pofuna kuteteza abambo ambiri ku nthendayi.

Related posts

Gulu la Bwaila lapereka thandizo kwa aulumali

Alinafe Mlamba

A polisi awombera wakuba ku Blantyre

Alinafe Mlamba

Ntchito yomanga malo opereka madzi ku Mangochi yafika theka – SWRB

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.