Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Awanjata pogulitsa mankhwala owopsa

Anthu asanu ndi awiri awatsekera ku polisi ya Ntcheu atawagwira akugulitsa mankhwala owopsa ophera tizilombo monga anankafumbwe mopanda chiloleza m’misika m’bomali.

Mmodzi wa akuluakulu ku bungwe la Pesticides Control Board, a Benson Kaphandira, ati mankhwalawa omwe ndi amapilisi komanso ena amadzi, ndi owopsa kotero kuti akuvulaza komanso kupha anthu ochuluka.

Mneneri wa apolisi ku Ntcheu, a Jacob Khembo, ati anthu  omwe awamangawa, akuyankha milandu yogulitsa mankhwala owopsa popanda chilolezo komanso kugulitsa mankhwala osavomerezeka.

Iwo ati ntchitoyi ipitilira pothana ndi mchitidwewu.

Related posts

Immigration, ACB akufuna kuthetsa ziphuphu

Romeo Umali

CRWB NEEDS 1.2 TRILLION KWACHA TO ADDRESS WATER CHALLENGES

Romeo Umali

Atsogoleri azipembedzo alimbikitsa bata

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.