Malawi Broadcasting Corporation
Development Environment Local Local News Nkhani

Alimbikitsa anthu kupha makwacha kuchokera ku zinyalala

Mmodzi mwa akuluakulu ku bungwe lowona zakasamalidwe kazinyalala la Waste Advisors, a John Chome, ati dziko la Malawi lili ndikuthekera kopeza phindu lochuluka kuchokera ku zinyalala.

A Chome anena izi mumzinda wa Lilongwe pamene amafotokozera atolankhani pazokonzera za msonkhano wawo waukulu wolimbikitsa anthu kasamalidwe kazinyalala, omwe udzachitike pa 27 March chaka chino ku Bingu International Convention Centre (BICC) mumzinda wa Lilongwe.

A Chome ati anthu akuyenera kusintha kaganizidwe kuti zinthu zakutha ntchito sizingagwirenso ntchito, ndipo anati kaganizidwe kotere kakuthandizira kuwononga chilengedwe.

“Zinyalala za pakhomo monga zakudya zotsala, makoko ambatata ndi zina zimapanga manyowa amphanvu omwe angathandize kubwezeretsa chonde mnthaka,” anatero a Chome.

Bungwe la Waste Advisors likugwira ntchito ndi a mabungwe, ochita malonda, makhonsolo mwa ena pofuna kudziwitsa anthu phindu lomwe lingapezeke kuchokera ku zinyalala.

 

Related posts

BANK DONATES TOWARDS MALAWI LAW SOCIETY AGM

Rabson Kondowe

MINISTRY INTENSIFIES FIGHT AGAINST CORRUPTION

McDonald Chiwayula

Centenary Bank to drill customers on financial literacy

Yamikani Simtowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.