Timu yadziko lino ya anyamata osapitilira zaka 20 yatuluka mu mpikisano wachaka chino wa COSAFA pamene yagonja masewero otsiriza ndi Lesotho 3-2.
Hermas Masinja ndi Mwisho Mhango ndi omwe anagoletsera Malawi.
Malawi yapambana masewero amodzi kugonja kawiri ndipo yatsilizira panambala yachitatu mu gulu C.
South Africa ndi yomwe yatsogola mugululi ndi mapointi 9 ndipo yadzipezera malo mu ndime yamatimu anayi otsiriza.
Matimu ena amene afika mundimeyi ndi Zimbabwe, Angola ndi Zambia.
Matimu awiri omwe afike mundime yotsiriza ndi omwe adzayimire COSAFA kumpikisano wa Africa Cup of Nations.
Olemba : Praise Majawa