Apolisi ku Chileka mumzinda wa Blantyre ati akufufuza chomwe chapha mwana wamwamuna wazaka zitatu atadya chinangwa chophika chomwe akuchiganizira kuti chinali ndi mankhwala okupha.
Ofalitsankhani wapolisi ku Chileka, Jonathan Phillipo, wati mlongo wake wa malemuyo anaphika chinangwa kenako ndikuchisiya pamoto iye ndikuchokapo.
Atabwera, mtsikanayo anagawa chinangwacho kwa ana anzake a mnyumbamo ndikuyamba kudya. Ndipo mayi a anawo, Bernadetta Magombo wazaka 32, omwe anachokapo, anapeza anawo akusanza. Mayiwo anathamangira ndi anawo kuchipatala komwe mwana mmodziyo wamwalira ndipo ena anayi awagoneka pachipatala cha Mdeka komwe akulandira thandizo la mankhwala.
Pakadali pano, apolisiwo ati akuyembekezera zotsatira za chipatala kuti adziwe chomwe chapha mwanayo.