Wapampando watsopano wa bungwe loyendetsa zisankho la MEC, Justice Annabel Mtalimanja, alumbilitsidwa lachisanu pa 21 June, 2024 ku Lilongwe High court nthawi ya 9 koloko m’mawa.
Ofalitsankhani wa MEC, a Sangwani Mwafulirwa, wati ma Komishonala awiri atsopano omwenso asankhidwa: M’busa Phillip Kambulire ndi Dr. Limbikani Kamlongera alumbiritsidwanso pa mwambowu.
Olemba: Blessings Cheleuka