Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yati idzasakha mphunzitsi watsopano gawo loyamba la super league likatha ndipo yati yemwe akugwirizira udindowu Meke Mwase ali ndi mwayi waukulu otengeratu ntchitoyi.
Mwase akuthandizidwa ndi Bob Mpinganjira kutsatira ndipo adatenga udindowu pambuyo pa kutula pansi udindo kwa Nsazurwimo Ramadan.
Mkulu watimuyi, Panganeni Ndovi, wati aunikira mmene aphunzitsi ogwirizirawa agwilira ntchito gawo loyamba likatha.
Motsogozedwa ndi Mwase, timuyi yapambana masewero ake onse awiri.
Wandereres ili panambala yachitatu mu ligi ndi ma pointi 18.
By Praise Majawa