Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

UNICEF ipitiliza kuthandiza Mtukula Pakhomo

Bungwe la UNICEF lati ndilokondwa ndi momwe ntchito za ‘Mtukula Pakhomo’ zikuthandizira kuchepetsa umphawi mmakomo ambiri mdziko muno.

Yemwe akuyimira bungweli kuno ku Malawi a Shadrack Omol ayankhula izi pomwe amawonelera ntchito yolemba anthu ena omwe akulowa nawo mundandanda olandira ‘Mtukula Pakhomo’ ku Doroba kwa mfumu yaikulu Ntwalo ku Mzimba.

Iwo ati bungwe lawo lipitiriza kupereka thandizo kuntchitoyi ati chifukwa anthu ambiri akupindula ndi ntchitoyi.

Mmodzi wa akuluakulu ku unduna owona zosamalira anthu a Laurent Kansinjiro ayamikira bungwe la UNICEF chifukwa linayamba kuthandiza ntchito ya ‘Mtukula Pakhomo’ m’chaka cha 2006 pomwe ntchitoyi inkayamba.

Padakali pano anthu oposa 1,500,000 ndiomwe akulandira ‘Mtukula Pakhomo’ mdziko muno.

Wolemba: Henry Haukeya

Related posts

‘Palibe chiopsezo chilichonse’

Alinafe Mlamba

Zotsatira za mayeso a sitandade 8 ndi fomu 2 zatuluka

Alinafe Mlamba

Prezident Chakwera wafika pa Kaphuka Trading Centre ku Dedza

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.