Malawi Broadcasting Corporation
Health Local Local News Nkhani

Unduna wa za umoyo ndi okhudzidwa ndi kuchuluka kwa matenda a mu ubongo

Unduna wa za umoyo wati ndi okhudzidwa ndi kuchuluka kwa matenda amu ubongo m’dziko muno zitadziwika kuti anthu 281 ndi amene adzipha kuyambira mwezi wa January mpakana June chaka chino.

Chaka chatha nthawi ngati yomweyi, anthu 527 ndi amene anadzipha.

Mkulu oyang’anira matenda osapatsirana komanso amu ubongo ku undunawu, Dr Jonathan Chiwanda, ndi amene ananena zimenezi mu mnzinda wa Lilongwe pa msonkhano wa akuluakulu komanso ma bungwe omwe amaona za matenda a muubongo.

Bungwe la Global Health Corps ndi limene lathandizira ndi ndalama kuti msonkhanowu uchitike.

Dr Chiwanda anati msonkhano umenewu ndi ofunika zedi chifukwa adindowa aunika magawo ofunikira ndi kukambirana za momwe angagwilire ntchito zawo pofalitsa uthenga wa matenda amu ubongo moyenera.

Mkulu wa bungwe la Global Health Corps, a Simon Simkoko, ati ali ndi chiyembekezo kuti pakhala ubale wabwino komanso mgwirizano pakati pa ma bungwe omwe amaona za matenda amenewa kuti vutoli lichepe m’dziko lino.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CHAKWERA MEETS ILO CHIEF

Blessings Kanache

SCTP boosts livelihoods in Nkhata Bay

MBC Online

SADC extends SAMIDRC mandate

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.