Boma la Britain lathandiza chikonzero cha nyimbo la Lake of Stars ndi ndalama zokwana pafupifupi K169 miliyoni ngati mbali imodzi yolimbikitsa ubale pakati pamaiko awiriwa.
Kazembe wadziko la Britain kuno ku Malawi a Fiona Ritchie alengeza izi lero pomwenso kwangotsala masiku ochepa kuti phwandoli lichitike.
A Ritchie ati thandizoli ndilofuna kusintha chithunzithunzi chomwe chilipo maka chongothandizana panthawi ya zovuta komanso kulimbikitsa ubale wamaikowa komanso kutukula nkhani zamsangulutso.
Phwandoli likubwera patatha zaka zinayi lisakuchitika.
A Sharmila Elias ndi mkulu yemwe akuyendetsa phwando la Lake of Stars ndipo wayamikira boma la Britain kamba kathandizoli.
Phwando la oimba la Lake of Stars lomwe lichitike kwamasiku atatu m’mboma la Nkhotakota lichitika pokondwekeranso kuti lakwanitsa zaka makumi awiri tsopano chiyambire kusangalatsa anthu ndi kutukula oyimba mdziko muno powapatsa danga loonetsa luso lawo Ku dziko lonse.