Chinthuzi: UNICEF
Sukulu ya za ukachenjede ya Malawi University of Science and Technology (MUST) yatumiza akatswiri oulutsa tindege touluka tokha mlengamlenga kuti akathandize ndi ntchito yofunafuna ndege yomwe wakwera wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Saulos Chilima ndi anthu ena.
Ofalitsankhani wasukuluyi, a James Mphande, wauza MBC kuti tindegeti, tomwe timadziwika kuti ma Drones mchingerezi, tilipo toposa tisanu ndipo tikathandiza kwambiri chifukwa tidzikajambula dera lalikulu kwambiri mukanthawi kochepa.
A Mphande ati akatswiriwa anyamuka lero madzulo kupita m’chigawo chakumpoto.
Ndege yomwe wakwera wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu, yomwe inabwelera italephela kutera pa bwalo la ndege la Mzuzu, akuyiganizira kuti yasowa mu nkhalango ya Chikangawa chifukwa cha kuipa kwa nyengo.