Bungwe la Malawi Red Cross Society (MRCS) lapereka madzi a m’mipopi kwa anthu a m’dera la mfumu yayikulu Mwirang’ombe m’boma la Karonga pofuna kulimbikitsa ukhondo.
Madziwa ndi odalira mphamvu ya dzuwa ndipo pali mipopi 16 yomwe yayikidwa m’malo osiyanasiyana.
M’modzi mwa akuluakulu abungweli, a Dan Nyirenda, ati madziwa afikira mabanja 480 kuphatikizapo sukulu ya pulayimale ya Ngara, chipatala cha ching’ono cha m’deralo komanso malo ochitira malonda.
Yemwe anayimira Bwanamkubwa wa bomali, a Yaz Nyirenda, anati anthu m’derali amavutika kaamba kosowa madzi abwino ndipo thandizoli lithetsa vutoli.
M’modzi mwa amayi okhala m’mudzi mwa agulupu a Muyeleka, a Watipaso Simeza, anathokoza chitukukochi.
“Poyamba timatenga madzi kunyanja komwe ndi kutali komanso madziwo sanali awukhondo,” a Simeza anatero.
Chifukwa chosowa madzi awukhondo, chaka chatha chokha anthu 63 akhala akugwidwa ndi nthenda ya Cholera ndipo asanu ndi awiri anafa ndi nthendayi.
Olemba: George Mkandawire