Nthambi yoona za nyengo m’dziko muno yatsimikiza kuti namondwe Filipo safika m’dziko muno.
Nthambiyi yati namondweyu akuyenda mobwelera ku nyanja ya mchere ya India, komwe ndi kotalikirana ndi malo okhala anthu.
M’mbuyomu, iwo adaalengeza kuti chiopsezo cha namondweyu ndi chochepa koma mpweya opepuka pa nyanja ya mchere ulimbikitsa kugwa kwa mvula m’madera ambiri m’chigawo cha kum’mwera kuyambira Lamulungu mpakana lero Lachitatu.
Ngakhale zili chomwechi, nthambiyi idaikiratu zipangizo zothandiza kupulumutsa anthu ngati ngoziyi ingachitike, mogwirizana ndi a Red Cross, asilikali a Malawi Defence Force ndi a Marine Department.