Pamene anthu a m’boma la Ntchisi akulandira ndalama za Mtukula Pakhomo, banja la a Mvula lalangiza anthu kuti azigwiritse ntchito mwanzeru monga kuchita malonda ang’ono ang’ono kuti athandizike kwa nthawi yayitali.
Banjali lili kwa mfumu yayikulu Kalumo m’bomali ndipo lati iwo anayamba kulandira ndalamazi m’chaka cha 2018, zimene zidawathandizira kuyikitsa magetsi m’nyumba yawo, kupititsa ana awo kusukulu ndi kugula ziweto.
Kuonjezera apo, iwo atinso anthu onse olandira ndalamazi adzifunsira nzeru kwa anthu ena amene akupindula ndi ndalama za Mtukula Pakhomo.
Mfumu Kalumo nayo yalangiza anthu olandira ndalamazi kuti asamazimwere mowa ndi kuchitira njuga.