Malawi Broadcasting Corporation
Business Local Local News Nkhani

‘Tiganizireni poonjezera ndalama za mtukula pakhomo’

Anthu omwe akupindula ndi ndondomeko ya boma ya mtukula pakhomo m’boma la Chitipa apempha boma kuti liwonjezere ndalama zomwe amalandira kuti adzitha kuthandidzira mabanja awo mosavuta.

Anthuwa anena izi pomwe komiti yaku nyumba ya malamulo yoona za ulamuliro wabwino imayendera ena mwa anthu omwe akupindula ndi ndondomekoyi m’bomali.

Olive Kasisi omwe ali ndi zaka 61 ati ngakhale apindula ndi ndondomeko ya mtukula pakhomo, mpofunika kukweza ndalama zomwe amalandira kuti athe kupitiliza kuthandiza banja lawo.

Ndipo mlembi wamkulu ku unduna owona za chisamaliro cha anthu, a Nwazi Mnthambala, wati pempholi ndi lomveka ndipo atsimikiza kuti undunawu unapereka kale ganizo lotere kwa adindo.

Mabanja 4,474 ndi omwe akupindula ndi mtukula pakhomo m’boma la Chitipa momwe muli anthu oposa 25,000.

Olemba: George Mkandawire

Related posts

Machinga farmers to plant 50,000 trees

Romeo Umali

Maso Awards eyes international platform

Romeo Umali

Balaka residents concerned over environmental, health risks from mining activities

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.