Ofesi yoona zofalitsa nkhani mu ofesi ya mlembi wamkulu wa boma ndi nduna OPC yalangiza atolankhani kuti apitirize kugwira bwino ntchito ndi boma.
Mneneri wa ofesi yi, a Robert Kalindidza ndiomwe anena izi ku Mulanje pamsonkhano waukulu wapa chaka wa atolankhani achikatolika m’dziko muno.
A Kalindidza ati atolankhani amagwira ntchito yayikulu yofalitsa mauthenga ndi ndikuzindikiritsa anthu kotero ndi bwenzi leni leni la boma pa chitukuko.
Poyankhulapo, wachiwiri kwa wamkulu wa bungweli mayi Josephine Chinele ati bungwe la Association of Catholic Journalists-ACJ lachita zinthu zochuluka pothandidza pa chitukuko chadziko lino monga kuthandidza anthu ovutika munthawi ya ngozi zogwa mwadzidzi