Bungwe la National Water Resources Authority lati lili ndi mapulani omanga zipilala zomwe zithandize kuletsa anthu kumanga zinthu zosiyanasiyana m’phepete mwanyanja.
Mkulu wabungweli, a Dwight Kambuku, alankhula izi kutsatira kukwera kwa mlingo wamadzi mu nyanja ya Malawi, zomwe zachititsa kuti nyumba ndi zinthu zina zomwe anthu anamanga m’mbali mwanyanjayi zikhale zili mmadzi.
A Kambuku atsindikanso kuti bungwe lawo silinatseke Kamuzu Barrage ku Liwonde monga momwe anthu akhala akunenera kuti kutseka kwa pamalowa ndikomwe kwachititsa kuti mlingo wamadzi ukwere mnyanja ya Malawi.
“Ndikulakwa kumanena kuti bungwe lathu latseka Kamuzu Barrage popeza, mwa zina, madzi omwe amadutsa pa Kamuzu barrage amawagwiritsa ntchito popanga magetsi komanso Southern Region Water Board ndi Blantyre Water Board amakhala akupopa madziwa ndikugawira anthu,” anatero a Kambuku.
Pofika lachitatu, madzi akuti afika mlingo wa mamita 476.3.