Bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana la NICE Public Trust ku Mangochi lapempha omwe analembetsa mkaundula wa vote kuti asamale ziphaso zawo zovotera kuti adzakhale ndi mwayi oponya nawo voti yosankha atsogoleri akumtima kwawo.
Mkulu woona zofalitsa nkhani ku bungweli m’boma la Mangochi, a Joseph Chamambala, amalankhula izi mdera la Senior Group Makumba, mfumu yaikulu Chowe, pamsonkhano olimbikitsa bata ndi mtendere komanso kulolerana pamene dziko lino likuyembekezeka kuchita chisankho chosankha adindo osiyanasiyana.
“Munyengo ino andale ena amabwera kudzakunyengelerani kuti muwapatse ziphaso zanu zovotera, zimenezi musalole kumbukirani kuti kupereka chitupa chovotera munjira yotere ndi mlandu,” iwo anatero.
Pamsonkhanowu, bungweli lalimbikitsanso mafumu kuti athandizire pantchito yoonetsetsa kuti mmadera mwawo simukuchitika ziwawa zokhudza ndale.
Iwo ati izi zingatheke ngati mafumuwa akupereka mwayi kwa wina aliyense kuchita misonkhano yandale kuti anthu omwe adzaponye voti amve mfundo zomwe adindowa ali nazo tsiku la chisankho lisanafike.
Mmau ake, Senior group Makumba yati uthenga omwe bungwe la NICElapereka mderali wafika mu nthawi yake ndipo uthandizira anthu kutenga nawo gawo pa chisankho cha pa 16 Septermber.
Olemba: Owen Mavula