Katswiri wampira wamiyendo wadziko lino Tabitha Chawinga walandira mendulo ngati osewera mogometsa m’mwezi wa February 2024 mu ligi yayikulu ya mpira wa miyendo ya amayi m’dziko la France.
Chawinga anayamikira anzake amene amasewera nawo ku timu yake ya Paris Saint-Germain (PSG) Féminines,ponena kuti ndiwo apangitsa kuti apeze mphothoyi.
Msungwanayu akutsogola pa m’ndandanda wa omwetsa zigoli mu ligiyo, atamwetsa zigoli zakwana 13 pa masewero 17.
Aka ndi koyamba kuti katswiriyu alandire menduloyi.