Katundu yemwe bungwe la Malawi Council for Disability Affairs (MACODA) limayenera kugawa kwa anthu ovutika mdera la Mtanga kwa mfumu yaikulu Chimwala Ku Mangochi wakokoloka ndi madzi galimoto lomwe linanyamula katunduyo itasiya nsewu ndikugwera ku phompho chifukwa cha mvula yamphamvu komanso yamphepo yomwe yagwa ku Mangochi usiku wapa 12 November, 2024.
A Esnarth John, omwe anaona ngoziyi ikuchitika ati “dalaivala wagalimotoli anazindikira kuti zinthu sizili bwino ndipo anaima ndi kutsika koma atangotsika galimotolo linatengedwa ndi madzi komanso mphepo yamphamvu kukagwera kumsi kwa mlatho,” anatero a John.
Katunduyu ndi monga njinga 21 za anthu olumala komanso zina zofunikira kwa anthu awulumali osiyanasiyana.
Padakali pano ofalitsankhani ku khonsolo ya Mangochi, a Bishop Witmos auza MBC kuti ofesi yawo yalandira madandaulo kuti mabanja opitilira 300 akusowa pokhala madenga anyumba zawo ataonongeka ndi mphepo.
“Tili mkati mofufuza kuti tidziwe chiwerengero chenicheni chifukwa madera enanso ku Mangochi kuno akhuzidwa,” atero a Witmos.
Zimene MBC yawona ndizakuti anthu ambiri akusonkhana malo osiyanasiyana chifukwa akusowa pokhala.