A khonsolo yamzinda wa Lilongwe, mogwirizana ndi asilikali achitetezo, agumula ndikusalaza sitolo zimene zinaamangidwa mphepete mwa manda ku dera la Nsungwi ku Area 25 ku Lilongweko.
Malinga ndi anthu amene atitsina khutu, izi zachitika kum’bandakucha walero loweruka.
M’mbuyomu, anthu okhala mderali adakachita zionetsero ku ofesi za khonsolo yamzindawu ndikuopseza kuti achitapo kanthu ngati akuluakulu akhonsoloyi sakagwetsa sitolozi.
Iwo ankadandaula kuti sitolozi zidamangidwa kufupi kwambiri ndi manda.
Kanema: Social media
#MBCOnlineServices