Phungu wa kummawa kwa boma la Dowa a Richard Chimwendo Banda omwenso ndi Nduna yazamaboma aang’ono ayamikira mtsogoleri wa dziko lino poonetsetsa kuti chitukuko chikufika m’madera onse a m’dziko muno.
A Chimwendo Banda ayankhula izi pomwe mtsogoleri wa dziko lino akuyembekezeka kukaona momwe ntchito yomanga nyumba za asilikali a nkhondo zokwana 40 ku Mvera Support Battalion mdera lawo ikuyendera.
A Chimwendo Banda ati Dr Chakwera akukwanitsa malonjezo awo ndipo ati nzosangalatsa kuti chitukuko ngati ichi chikuchitika mmadera onse a mdziko muno.
“M’mbuyomu nyumba zing’onozing’ono ndi zomwe amamanga zoti makolo akakhala ndi ana awiri atatu amadera nkhawa kuti anawa adzigona pati ena mpaka kumagona pa balaza koma taonani nyumbazi za maofisala zokongola komanso nyumba za bwino kwambiri,” atero a Chimwendo Banda.
Iwo atinso dziko lino tsopano lanyamuka ndipo zipatso zomwe aMalawi akhala akuzifuna zibala mmagawo osiyanasiyana monga chitukuko cha zomangamanga, milatho komanso ku ulimi mwa zina.
Boma likumanga nyumba za asilikali zokwana 10000. Zina mwa izo 4000 ndi za apolisi zina 4000 ndi za asilikali ankhondo ndipo nthambi za asilikali a kundende komanso oona zotuluka komanso kulowa mdziko muno alandira nyumba 1000 nthambi iliyonse.
Wolemba: Beatrice Mwape ndi McDonald Chiwayula.
#mbcmw
#mbcnews
#mbconlineservices