Chipatala cha Zomba Mental chati chili ndi anthu 27 amene anamaliza kulandira thandizo la mankhwala koma amakanika kuti atuluke chifukwa abale awo amawakana.
A Harry Kawiya, ofalitsankhani wa chipatalachi, ndiwo amanena izi pamene amayendera malowa pamodzi ndi olembankhani kuti aone m’mene iwo akugwilira ntchito.
A Kawiya adalangiza anthu amene abale awo anasowa pakale kuti akafufuze ku chipatalachi chifukwa ena mwa iwo akhala pa malowa kwa zaka zokwana khumi.
“Tili ndi ena omwe kwawo sitimakudziwa mpakana tinapereka maina malinga ndi madera omwe anachokera,” iwo anatero.
Mwa anthu 27 amene ali ku Zomba Mental, 17 ndi abambo ndipo khumi ndi amayi.
Chipatala cha malingaliro amuubongo cha Zomba chili ndi chiwerengero cha odwala choposa 400.
#MBCDigital
#Manthu