Nduna yoona za chisamaliro cha anthu, a Jean Sendeza, lero ikuyendera Hope Orphanage, m’boma la Mchinji kuti imve ena mwa mavuto amene ana komanso akuluakulu oyendetsa malo amenewa akukumananawo.
Pamalowa, pakukhala ana oposera 600, ndipo sapereka ndalama ina iliyonse.
Awa ndi malo amene Madonna, oyimba wa m’dziko la America, anatenga David Banda ndi kukhala mwana wake m’chaka cha 2008.
Pamalowa pali sukulu ya nursery, primary, sekondale komanso yophunzitsa ntchito za manja, monga kusoka, kuwotchelera komanso zomangamanga.
M’busa Thomson John Chipeta anakhazikitsa malowa m’chaka cha 1998.