Mtsogoleri wa dziko la Guinea-Bissau a Umaro Sissoco Embalo afika m’dziko lino mawa Lachisanu kudzapepesa imfa ya amene wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino Dr Saulos Chilima ndi anthu ena omwe anamwalira pangozi ya ndege yomwe inachitika mu nkharango ya Chikangawa ku Mzimba.
Chikalata chomwe atulutsa amu ofesi yoona nkhani zakunja kwa dziko lino chatsimikiza kuti President Embalo akudzakumana ndi President Dr Lazarus Chakwera.
Mtsogoleriyu akuyembekezeka kudzafika pa bwalo la ndege la Kamuzu International ku Lilongwe mma 10:35 am ndipo adzanyamuka m’dziko muno kubwelera kwawo mawa lomwelo mma 1:30pm.