President wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wafika ku Lilongwe, kuchokera ku Blantyre komwe anapita kukatsekulira chionetsero chazamalonda.
Pofika pa bwalo la ndege la Kamuzu International ku Lilongwe, President Chakwera analandiridwa ndi Mlembi wamkulu mu ofesi ya prezidenti ndi nduna zake, a Colleen Zamba ndi akuluakulu ena.
Dr Chakwera anaoneranso magule amene anavina amayi a zipani za Malawi Congress ndi UTM.
Olemba: Isaac Jali