Prezidenti wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wanyamuka ku Blantyre kubwelera ku Lilongwe atatsekulira chionetsero chazamalonda ku Chichiri Trade Fair grounds.
Wapampando wa chipani cha MCP m’chigawo chakummwera, a Peter Simbi, akuluakulu ena aboma komanso atsogoleri andale ndi mafumu ndi ena mwa omwe anapelekeza Dr Chakwera komanso First Lady Madam Monica Chakwera pabwalo la ndege la Chileka.
Olemba: Blessings Cheleuka