Popitiriza ndi ulendo wake m’chigawo chakummawa kwa dziko lino, Prezidenti Dr Lazarus Chakwera lero ayendera chitukuko chosiyanasiyana m’boma la Balaka.
Mtsogoleri wadziko linoyu ayendera Demeter Mega Farm ku Nkaya ndipo kenaka akayendera fakitale yopanga cement ya kampani ya Portland kwa mfumu yayikulu Nsamala ku Balaka komweko.
Kenaka, Dr Chakwera akakhala mlendo olemekezeka pamwambo okondwelera kuti bungwe logawa ngongole la NEEF tsopano lakwanitsa kugawa ngongole zokwana K1 billion.
Mwambowu ukuchitikira pa bwalo la zamasewero la Balaka.