Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Gwiritsani bwino ntchito feteleza wa ngongole’

Boma lalimbikitsa alimi m’dziko muno kugwiritsa bwino ntchito mwayi omwe awupeza wa feteleza wangongole kuchokera ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF), ponena kuti alimiwa ndiomwe athandize kuti dziko lino likhale ndi chakudya chokwanira.

Nduna yofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, anena izi ku Nanjiri m’boma la Lilongwe pamene bungwe la NEEF likupitiriza kupereka feteleza kwa alimi.

A Kunkuyu ati alimiwa asangokhala osangalala ndikulandira fetelezayu koma amugwiritse ntchito moyenerera pothira m’minda yawo.

Polankhula ku Nanjiri pogawa fetelezayu, Nduna ya zamalonda a Sosten Gwengwe, omwenso ndi phungu wa dera la Lilongwe Msozi North, anati zomwe zomwe akuchita a NEEF zili ndi kuthekera kothandiza dziko lino kukhala ndichimanga chochuluka ndipo likhoza kugulitsanso kumayiko ena, makamaka ngati alimi agwiritse bwino zipangizozi.

Mkulu wa bungwe la NEEF, a Humphrey Mdyetseni, ati ngakhale ntchitoyi idakali yambiri, ntchitoyi ikuyenda bwino ndipo nawonso alimi akukondwera ndi mmene ntchitoyi ikuyendera.

Mfumu yayikulu Kalumbu ya m’boma la Lilongwe yayamikira boma popereka ndalama ku bungwe la NEEF zogwirira ntchitoyi.

NEEF yati tsopano yapereka matumba oposa 100,000 kwa alimi mmadera osiyanasiyana m’dziko muno.

 

Olemba: Yamikani Makanga

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Musangodalira ulimi okha, bungwe la We Effect latero

Aisha Amidu

POLICE RESCUE MINORS, ARREST DEFILERS IN NIGHT RAID

MBC Online

Chakwera leaves for Malawi

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.