Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Fodya akadali ndi tsogolo lowala – Chithyola Banda

Nduna yoona zachuma, a Simplex Chithyola Banda, yabwerezanso kunena kuti fodya akadali imodzi mwa mbewu zofunikira kwambiri pachuma cha dziko lino.

Ndunayi yati ndikofunika kuti nthambi zonse zokhudzidwa, maka alimi a fodya, apitirize kulima mbewu yochuluka komanso motsatira njira zabwino pofuna kuti adzikolola fodya wapamwamba  yemwe angamagulitsidwe pa mitengo yabwino.

Nduna yoona zachuma, a Simplex Chithyola Banda

Polankhula pomwe bungwe la atolankhani wolemba za fodya la Media Network on Tobacco linakayendera Namuleri Farms m’boma la Kasungu, ndunayi inatsindika zakufunika koti mMalawi akhale ndi chidwi chotengapo gawo pa ntchito zaulimi, powonjezera zonse zomwe amachita mmoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Powonjezera fodya wa mitindu yosiyanasiyana, pa malowa amachitanso ulimi wa chimanga, nthochi, mpunga, chinangwa komanso waziweto monga mbuzi, nkhumba, ng’ombe komanso nsomba.

Mkulu wa Media Network on Tobacco, a Alfred Chauwa, ayi fodya ndi mbewu yomwe iyenera kutetezedwa ndi wina aliyense pozindikira kuti kufikira lero ndi yokhayo yomwe imabweretsa ndalama za mmaiko akunja zochuluka kwambiri kuposa mbewu iri yonse.

 

Olemba: Timothy Kateta

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Amugwira ataba makina opimila amayi apakati

Mayeso Chikhadzula

Musamvere andale abodza, ogawa mitundu — Chimwendo Banda

MBC Online

TUMBUKA HERITAGE ASSOCIATION EMBARKS ON DOCUMENTATION PROJECT

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.