Omenyera ufulu wa ana, a Amos Chibwana, ananenetsa kuti nkhanza zochitira ana m’banja aMalawi asamazilekelele kapena kuziyang’anira pansi.
Izi zili chomwechi pamene aPolice ya South Lunzu ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre atsindika kuti anamanganso bambo Chitala, amene akazi awo, a Linda Chitala, akhala akuzunza mwana omupeza wa bambowo. Mayiwo ndi amene anamangidwa koyambilira.
“Tiyamikire kuti nkhaniyo ikuyenda mwachangu. Tionenso kuti nkhaza yachitika ndi munthu wamkulu wamene amayenereka kuti ateteze mwana osati kumuzuza,” a Chibwana anatero.
Mkulu wa a Police ya South Lunzu, a Patricia Njawiri, anati iwo anatsegulira bambo Chitala mlandu olekelera nkhanza koma anawatulutsa pa belo tsiku lomwe anawamangalo.
“Tinawatulutsa chifukwa chakuti timafuna kuti akasamale ana ena omwe anatsala kunyumba kwawo chifukwa anawo anali okha ndipo sitimayenera kuwaphera ufulu koma bamboyu sitinathane nayebe,” Anatero a Njawiri.
Pothilaponso ndemanga ina, munthu winanso omenyera ufulu wa ana, a Jenipher Mkandawire, anayamikira apolisi pochita machawi kuti lamulo ligwire ntchito chifukwa anati nkhani zoterozo “zikunka nakulirakulira”.
A Linda Chitala akaonekera ku bwalo la milandu lolemba likudzali.