Billy Kaunda walangiza oimba kuti aphunzire kugwira ntchito ndi aluso ena monga alakatuli.
Kaunda wayankhula izi pomwe wati akubwera ndi chimbale chatsopano posachedwapa momwe Okoma Atani Malunga, katswiri pandakatulo, wamulembera nyimbo zingapo.
“Sikoyamba kugwira ntchito ndi a Malunga pankhani yanyimbo, anandipatsapo ndakatulo ya ‘Naliyera’ komanso ‘Mawu Angawa’ mwazina,” anatero Billy Kaunda.
Iye wati pakadalipano akutangwanika ndi ntchito zina monga zakunyumba yamalamulo ngakhale wati zokhudza chimbale chake zilimchimake.