National Bank of Malawi (NBM) yasaina mgwirizano ndi kampani za Sky Energy Africa komanso 265 Energy.
Mu mgwirizanowu, makasitomala a NBM adzigula katundu wa kampani ziwirizi kupyolera ku ngongole yomwe adzigwirizana ndi bankyi.
Poyankhula atasainila mgwirizanowo, m’modzi mwa akuluakulu a bankiyi, a Oswin Kasunda, anati mgwirizanowu upinduliranso ochita bizinesi zing’onozing’ono zomwe zinalibe kuthekera kogula katundu wa kampani ziwirizi kaamba kakuchepekedwa nthumba.
A Kasunda atinso mgwirizanowo uthandizanso kuteteza zachilengedwe kaamba koti katundu wa kampanizi amagwiritsa ntchito njira zambiri zachilengedwe monga dzuwa.
Olemba: Naomi Kamuyango