Malawi Broadcasting Corporation
Floods Local Local News Nkhani

Chaka chatha chichitikireni Namondwe Freddy

Lero pa 13 March, 2024 chaka chatha tsopano chichitikireni ngozi ya namondwe wa Freddy yemwe inapha anthu oposa 1000 komanso kuvulaza ambiri, anakokolola nyumba ndi katundu komanso anawononga zomangamanga za boma monga misewu, milatho ndi zipatala.

Awa ndi ena mwa makanema omwe MBC inajambula mu nthawiyi chaka chatha.

Kanema ali pansiyu, akuonetsa m’mene namondwe Freddy adaonongera msewu wa Chiladzulu.

 

Kanema ali m’musiyu akuonetsa m’mene zinalili mu mzinda wa Blantyre, pansi pa phiri la Soche.

Namo mu mzinda wa Blantyre Namondweyu adaononga kwambiri.

Nyumba nazo zidaonongeka kaamba ka namondweyu, monga m’mene kanema ali m’musiyu akuonetsera madzi atalowa m’nyumba ina ya ku Chilobwe.

A Abida Mia, nduna yo oona za madzi komanso ukhondo, adapita komweko ku kaona m’mene namondweyu adaonongera.

Namondweyu adaononga kwambiri minda ndi malo okhala anthu, ngati m’mene zilili mu kanema ali m’munsiyu yemwe akuonetsa m’mene kunalili ku Chiradzulu.

Ngakhale kunali ngozi, anthu ena adaonetsa mtima wa chikondi ngati m’mene adachitira bambo Bamusi Agentina omwe boma linawayamikira kaamba koti anapulumutsa asilikali a MDF omwe anakokoloka ndi madzi osefukira mu mtsinje wa Mkando m’noma la Mulanje.

Madzi osefukira adaoononga Mlatho wa Mkando ku Mulanje.

Mtsogoleri wa dziko lino, a Lazarus Chakwera kenako adapempha thandizo kwa maiko akunja ponena kuti ndalama zokwana 700 million Dollars ya America ndi imene imafunika kuti dziko la Malawi likonzenso zimene zidaoonongeka.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mining Minister seeks expert assistance

Emmanuel Chikonso

Dr Chakwera to visit Rumphi

MBC Online

Chawinga sisters in Scorchers’ strong COSAFA squad

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.