Ena mwa anthu amene amagwiritsa ntchito misewu ya mu mnzinda wa Lilongwe ati ndi okondwa ndi mmene ntchito yomanga misewu mu mnzindawu ikuyendera.
Poyankhula ndi MBC, a Biliati Basikolo amene amayendetsa minibus yoyenda ku Area 25 kupita mu tauni ya Lilongwe ati ndi wokondwa kuona momwe roundabout ya Amina yasinthira mu kanthawi kochepa munzindawu.
“Tikamayenda pena kumaona ngati tili kunja kwa dziko lino. Misewu yake ikukhala yapamwamba,” anatelo a Basikolo.
Malinga ndi malipoti, misewu imene ikumangidwa monga wa Mzimba Street, Kanengo-Crossroads ndi Kenyatta Drive ikhoza kutha mwachangu poyerekeza ndi mmene oyendetsa ntchitoyi amaganizira poyamba.
Mseu wa Kanengo-Crossroads akumanga ndi a kampani ya Shadong Liquao ya mdziko la China ndi thandizo la ndalama zoposa K22 billion.
Msewu wa Mzimba Street akumanga ndi a kampani ya Mota Engil.