Bungwe loona za madzi la Southern Region Water Board (SWRB) lati ntchito yomanga malo omwe adzipereka madzi kwa anthu okhala mmadera ozungulira Makanjira ku Mangochi tsopano yafika theka, kuchokera pomwe ntchitoyi inayamba mwezi wa July chaka chino.
Mkulu wa bungweli, a Duncan Chambamba, anena izi pamene komiti ya aphungu akunyumba ya Malamulo yoona za chilengedwe imayendera ntchito yomanga malowa yomwe akuitcha Makanjira Water Supply Project.
Malinga ndi bungweli, zina mwa ntchito zomwe zikugwilika pamalowa, ndikuika ma pipe omwe adzithandizira kupopa madzi kuchokera pa nyanja ya Malawi, kumanga malo osungila ndi kusamalira madzi asanapite mmipope komanso kumanga nyumba za ogwira ntchito.
Wapampando wa komiti ya aphungu akunyumba ya malamulo yoona za chilengedwe, a Welani Chilenga, ati komitiyi ndi yokhutila ndi momwe ntchito yachitukuko cha madzi ikuyendera pa malowa.
“Tadzionera tokha kuti ntchitoyi ikuyenda bwino koma kontalakitala wadandaula kuti kuchedwa kwa malipilo ndi limodzi mwa mavuto omwe akukumana nawo ndiye nkhani imeneyi tikaitula mmanja mwa unduna wa zachuma,”Atero a Chilenga.
Anthu pafupifupi 68,000 ndiomwe akuyembekezeka kupindula popeza madzi abwino m’derali, ntchitoyi ikatha pofika mwezi wa July chaka cha mawa.
Olemba Owen Mavula