Nthambi yoona za anthu ochoka mmaiko ena kukagwira ntchito ku Israel yatsimikizira anthu komanso boma la Malawi kuti aMalawi okagwira ntchito kumeneko adzikalandira ndalama zosachepera 1500 US dollars pa mwezi.
Mmodzi mwa akuluakulu ku nthambiyi, Raisin Sassan Shirley, wati chikufunika ndichakuti boma la Malawi lidzitumiza anthu odziwa ntchito, odzipereka komanso olimbikira.
Shirley wanena zimenezi ku Lilongwe atakambirana ndi a Unduna waza Ntchito zokhudza mgwirizano wa maiko awiriwa.
M’mbuyomu, maiko a Malawi ndi Israeli adamvana kuti anthu 500 apite ku Israel kukagwira ntchito za mminda ndipo malinga ndi a Shirley, mwayi uliponso wa nkhaninkhani wa ntchito zina kumeneko.
Mmawu awo, a Agnes Nyalonje, Nduna yaza Ntchito ati panopa boma lidzitumiza okhawo olimbika komanso a khalidwe labwino.
Iwo ati posachedwapa ayamba kuyendera anthu amene afunsira ntchitoyi pofuna kuwayesa ngati ali ndikuthekera kokatumikira ku Israel.
Olemba: Isaac Jali