Khwimbi la anthu lasonkhana pa Mtengowanthenga m’boma la Dowa, pamene akudikila mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, kuti awalankhule pamene iye akudutsa pa ulendo wake opita munzinda wa Mzuzu.
Polankhula pokonzekera mtsogoleri wa dziko linoyu, Village Headman Chigona, amene dzina lawo ndi a Petro Oposi, ati akuyamika boma chifukwa msika wa fodya wayenda bwino chaka chino, kaamba ka mitengo yabwino yomwe boma la Dr Lazarus Chakwera lidanenelera kwa ogula.
“Chaka chino mitengo ya fodya inali bwino kwambiri zomwe sizinachitikepo zaka zambiri zapitazi… Alimi apeza makwacha,” anatero a Oposi.
Iwo ayamikanso boma kaamba ka ntchito yokonzanso msewu wa M1, yomwe ili mkati panopa.
Olemba: Isaac Jali