Malawi Broadcasting Corporation
Crime Development Local Local News Nkhani

Akakhala kundende zaka 14 chifukwa chogwilira wamisala

Khoti lina ku Phalombe lalamula bambo wazaka 69, Amon Symon, yemwe amadziwikanso ndi dzina loti Henderson Helema, kukakhala ku ndende zaka 14 chifukwa chogwililira mtsikana yemwe amadwala matenda a mu ubongo.

Ofalitsankhani wapolisi ku Phalombe, Jimmy Kapanja, wati mkuluyo ananyengelera mtsikanayo ndikuchita naye zadama ku bafa.

Malinga ndi a Kapanja, mtsikanayo anafika kwawo zovala zake zitanyowa ndi madzi. Makolo ake atamufunsa, analongosola zomwe zinachitikazo ndipo anawonjezera kuti bamboyo anamuuza kuti asambe kenako adzipita, ndichifukwa chake ananyowetsa zovala.

Mayi a mtsikanayo anakanena ku polisi ya Chitekesa ndipo kukhoti, bamboyo anapempha kuti amupatse chilango chofewa chifukwa ati ndi wachikulire, zomwe woweruza milandu sanagwirizane nazo.

Symon ndi wa mmudzi wa Komihera, mfumu yaikulu Jenala m’boma la Phalombe.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Salima Sugar yayambanso kupanga Shuga

Tasungana Kazembe

Swahili, Portuguese inclusion in Malawi Syllabus on track, says Ministry of Education

Juliana Mlungama

ACB ARRESTS MWANAMVEKHA OVER PROCUREMENT SAGA

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.