Phungu wa kumpoto kwa boma la Mangochi, a Benedicto Chambo, wati ma boma a m’mbuyomu anamutaya ndipo sanalabadire ukadaulo wake pa ntchito za ulimi ndi zina zambiri.
A Chambo, amene ndi phungu wa chipani chotsutsa cha Democratic Progressive, anasankhidwa posachedwapa ndi mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera kukhala wachiwiri kwa nduna ya za ulimi.
Iwo anati ndi zosangalatsa kuti Dr Chakwera waona kuthekera kwawo pa ntchito imene anawapatsa.
“Ndinali kusalidwa koma Dr Chakwera wanditola ndili ndi chimwemwe chodzadza tsaya,” anatero a Chambo.
Pokambapo pa nkhani za chitukuko cha mdera mwawo, a Chambo anayamikira Dr Chakwera kaamba ka zitukuko monga misewu, madzi a ukhondo komanso za umoyo.
Iwo anati ayambitsa ntchito za ulimi wa mthilira pogula ma pump oyendera mphamvu ya magetsi a dzuwa, zimene akuzipeleka kwa achinyamata.
“Tikufuna kuti tithane ndi njala mdera langa polimbikitsa ulimi wa mthilira komanso kuchepetsa kudalira boma pa chilichonse,” anatero phunguyu.
A Chambo anatinso ndi odzipereka kutumikira boma la Chakwera kuti likwaniritse masomphenya a 2063.
Olemba: Grant Mhango