Bungwe la Malawi Network of Older Persons’ Organizations (MANEPO) lati ndi lokhudzidwa ndi kuchuluka kwa nkhanza zomwe achikulire akukumana nazo m’dziko muno kuphatikizapo kuwaganizira kuti ndi mfiti.
Mkulu wa bungweli, a Andrew Kavala amathilirapo ndemanga pa nkhanza zomwe zachitikira mayi Mary Laini a zaka 87 a mmudzi mwa Matewere kwa T/A Juma m’boma la Mulanje pomwe awanamizira kuti amamanga mvula.
A Kavala anati izi ndi kaamba ka umbuli komanso zikhulupiliro zopanda ntchito kuphatikizapo nkhani za ufiti zomwe anati ndi kuphwanya ufulu wa achikulire m’dziko muno.
M’chikalata chomwe atulutsa a bungwe la MANEPO, apempha a polisi kuti afufuze nkhaniyi ndi kumanga onse okhudzidwa, komanso kuyika ndondomeko zothandiza kuteteza ufulu wa achikulire m’dziko muno.
A bungweli ati akutsatira ndi chidwi kuti chilungamo chiwoneke kwa mayi Laini.
Olemba: Grant Mhango