Malawi Broadcasting Corporation
Development Local News

Nduna zaboma zikakhala nawo pamwambo oyika maliro m’maboma onse

Nduna ya zofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, yati mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera walamula nduna zake kuti zikakhale nawo ku mwambo woyika mmanda matupi a anthu omwe anafa pa ngozi ya denge pamodzi ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, malemu Dr Saulos Chilima.

A Kunkuyu ati anthu amene akupita m’boma la Ntchisi kuperekeza a Chisomo Chimameni akakhala ndi nduna ya za malimidwe a Sam Kawale ndi nduna ya za Chitetezo cha m’dziko, a Ken Zikhale Ng’oma.

M’boma la Kasungu kwawo kwa malemu a Lukas Kapheni kukakhala nduna ya za Umoyo Mayi Khumbize Kandondo Chiponda, Nduna ya za chuma a Simplex Chithyola Banda komanso nduna ya zomangamanga a Jacob Hara kuimilira mtsogoleri wa dziko lino Dr Chakwera.

Ndipo m’boma la Thyolo kumwambo woyika m’manda thupi la malemu Major Flora Selemani, nduna ya za masewero a Uchizi Mkandawire komanso wachiri kwa nduna ya za maphunziro, mayi Nancy Chaola Mdooko ndi omwe akayimilire Dr Chakwera.

M’boma la Zomba komwe kukachitikire mwambo oyika mmanda thupi la malemu Owen Sambalopa kukakhala wachiwiri kwa nduna ya zachitetezo, a Harry Mkandawire komanso wachiwiri kwa nduna ya za ma boma aang’ono, a Owen Chomanika.

Nduna ya za magetsi a Ibrahim Matola komanso nduna ya za malonda a Sosten Gwengwe ndi omwe akakhale nawo mmalo mwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Chakwera ku mwambo woika mmanda thupi la malemu Major Wales Aidini m’boma la Mangochi.

Ndipo m’boma la Lilongwe kwawo kwa malemu Daniel Kanyemba kukakhala Mayi Vera Kantukule nduna ya zokopa alendo komanso Mayi Liana Kakhobwe Chapota wachiwiri kwa nduna ya za ukhondo.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Storm damages property in Nsanje

MBC Online

GMT, COMFWB assure women entrepreneurs of support

Yamikani Simutowe

MANEB halts certificate services ahead of exams

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.