Mwambo wa mapemphero uli mkati ku nyumba yachisoni ya Sunset ku Kanengo, omwe ndi mwambo wofuna kuperekeza matupi a omwe adamwalira pa ngozi ya ndege ku Chikangawa m’boma la Mzimba.
Ena mwa akuluakulu apolisi komanso asilikali ankhondo afika kale pamalopa, kuphatikizapo mkulu wa Polisi m’dziko muno, mayi Merlyn Yolamu, nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ndi wachiwiri kwa sipikala wa nyumba ya malamulo, a Madalitso Kazombo.
Mwambowu ndi wa malemu Colonel Owen Sambaluka, Major Flora Selemani Ngwirinji ndi Major Walesi Aidini amene amagwira ntchito ku Malawi Defence Force ndipo a Lukas Kapheni ndi a Inspector Chisomo Chimaneni amagwira ntchito ku Police.