Mtsogoleri wakale wadziko lino, Professor Peter Mutharika, wapempha anthu m’dziko muno kuti adzitenga mbewu zina ngati chakudya mmalo momangodalira nsima.
A Mutharika anena izi pa mwambo wachaka chino wa Mulhako wa Alhomwe omwe umachitikira ku likulu la Alhomwe kwa Chonde m’boma la Mulanje.
Iwo anati makolo akale ankadalira mbewu za mapira, chinangwa ndi mbatata, mwa zina, ngati chakudya ndipo samakhala ndi njala kwambiri. Iwo anaonjezeranso kuti mbewuzu sizifuna mvula yambiri, zimene zili zogwirizana ndi momwe mvula ikumagwera masiku ano.
Pamwambowu, mtsogoleri wakaleyu anapemphanso achinyamata kuti adzilimbikira maphunziro chifukwa angawathandize ku khala ndi tsogolo labwino ndiponso anapempha anthu m’dziko muno kuti adzilemekeza achikulire.
Chaka chino, mwambowu umachitikira pamutu wakuti “Mgwirizano wa cholinga chimodzi”.