Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Politics

Ndale zoopsyezana n’zosaloledwa — MCP

Mkulu oyang’anira ndale ku chipani cha Malawi Congress (MCP), a Maxwell Thyolera, ati ndale zoopsyeza ena, zimene anati akupanga a zipani zina ndi zosaloredwa mu democracy.

A Thyolera anena izi pa msonkhano wa chipani cha MCP umene ukuchitikira kwa Mgona ku Lilongwe.

M’modzi mwa akuluakulu a MCP, a Ken Msonda, analangiza anthu kuti akhale tcheru komanso asamangomvera zonena za atsogoleri andale ena omwe anati sangathandize dziko lino mu njira ina iliyonse.

A Msonda anaonjezeranso kuti boma lakale lidazunza kwambiri mtsogoleri wakale, Dr Bakili Muluzi, ndipo anati ndi zodabwitsa kuti anthuwo akufuna atakhala pa mgwirizano ndi chipani cha United Democratic Front pokonzekera chisankho cha chaka cha mawa.

Olemba: Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Japan to help upscale Malawi’s agriculture

Madalitso Mhango

‘Tikufuna changu pantchito zachitukuko’

Mayeso Chikhadzula

Let us all embrace a spirit of Umunthu — President Chakwera

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.