Munthu mmodzi wavulala modetsa nkhawa pa ngozi ya sitima ku Blantyre mu njanji ya Magalasi – Nyambadwe – kudutsa ku Chapima.
Ofalitsankhani za polisi ya Ndirande, a Maxwell Jailosi, ati adakafufuzabe za nkhaniyi ndipo a kampani ya CEAR, omwe ndi eni sitimayi, sanapezeke kuti ayankhulepo pa nkhaniyi.
Koma malinga ndi anthu amene akuti anawona ngoziyi ikuchitika, munthuyu anadumpha mu sitimayi, yomwe inali ikuyenda, pamene ena akuti amayesera kukwera sitimayi ikuyenda.
Munthuyu akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha QECH.
Olemba: Blessings Cheleuka