Bungwe la atsogoleri azipembedzo zosiyanasiyana m’dziko muno la Religious Leaders Organisation lapempha anthu kuti adzikhala mwabata nthawi zonse ndi kulemekeza atsogoleri adziko.
Mtsogoleri wabungweli, Sheikh Muhammad Chindamba, walankhula izi ku Lilongwe pamsonkhano omwe anakonza opemphelera dziko komanso kusankha adindo a abungweli.
Iwo ati ndizomvetsa chisoni kuti atsogoleri azipembedzo ena, omwe ntchito yawo ndikukhazikitsa bata ndi mtendere, akumayankhula mobweretsa chisokonezo, maka pamasamba a mchezo.
Iwo ati ndikofunika mtsogoleri wachipembedzo aliyense awonetsetse kuti akulimbikitsa umodzi ndi mtendere.