Msonkhano wa bishop a maiko a Malawi, Zambia komanso Zimbabwe watha m’boma la Salima pomwe agwirizana zogwilira limodzi komanso kutumikira mokomera nkhosa zao maikowo pa ntchito yazaumoyo, maphunziro komanso zosamalira zachilengedwe.
Msonkhano-wu avomereza mfundo zoyendetsera gululi lomwe tsopano azilitcha kuti Association of Catholic Bishops in Zambia, Zimbabwe and Malawi.
Powerenga mfundozo, prezidenti wa mabishop M’Malawi muno Archbishop George Desmond Tambala ati mwa zina agwirizananso zoti likulu laguli likhale ku Lusaka mdziko la Zambia ndipo wapampando wake tsopano akhala mtsogoleri wa dziko la Zimbabwe.
Msonkhano wina ngati omwewu udzachitika mchaka cha 2027 mdziko la Zimbabwe.